Popeza kuti citsimikizo ca khalidwe loyenera la munthu mu banja lonse ndico tsinde la ufulu, ungwiro ndi mtendere pa dziko liri lonse la pansi,
Popeza kuti kusalabadira ufulu wa munthu kwabweretsa khalidwe la nkhalwe pa umoyo wa munthu, ndi kutinso kusintha kwa zinthu pa dziko la pansi mwakufuna kupereka ufulu weni-weni pa umoyo wa munthu aliyense ndilo funo la munthu wamba aliyense,
Popeza kuti ndi kofunikira kuti ufulu wa munthu ucinjirizidwe ndi lamulo pofuna kupewa nkhondo yomenyera ufulu kukhala ngati njira yomwe munthu angagwiritse nchito pofuna kumasulidwa ku nsinga za nkhalwe,
Popeza kuti ndi kofunikira kukweza umodzi pakati pa mitundu ya maiko osiyana-siyana pa dziko lonse la pansi,
Popeza kuti anthu a m' maiko amene ali mamembala a bungwe la United Nations anabvomereza za kufunikira kwa ufulu wa munthu mu makhalidwe ace onse ndiponso kuti sipayenera kukhala kusiyana pakati pa mwamuna ndi mkazi m' makhalidwe ao ndikutinso maikowa anadzipereka kukweza nchito za cisangalalo ndi makhalidwe ena pa ufulu wa munthu,
Popeza kuti maiko amene ali mamembala a bungweli la United Nations anatsimikiza kugwirizana ndi bungweli pa nchito zokweza ufulu wa munthu pa umoyo wace ndi kutsatira zofunikira zonse mu lamuloli lopereka ufulu weni-weni pa umoyo wa munthu,
Popeza kuti kumvetsetsa cifuniro ca kufunika kwace kwa ufulu wa munthu pa umoyo wace kuli kofunikira kwambiri pofuna kuti cibvomerezoci cigwire nchito yace moyenera.
Motero tsopano, bungwe lalikulu la General Assembly likulengeza
Chibvomerezoci pakati pa imitundu ya antu onse a dzikoli la pansi, ndikuti munthu aliyense mokumbukira chibvomerezoci nthawi zonse adzakhoza kuthandiza kukweza ndi kukwaniritsa lamuloli pakati pa maiko onse amene ali mamembala a bungwe la United Nations ndiponso ku anthu okhala m' maiko ena amene sakhudzidwa ndi nchito za bungweli pa dziko lonse la pansi.
Anthu onse amabadwa mwa ufulu ndiponso olinganga m' makhalidwe ao. Iwo amakhala ndi nzeru za cibadwidwe kotero ayenera kucitirana zabwino wina ndi mnzace.
Munthu aliyense ali ndi danga lokhala ndi ufulu onse ofunikira pa umoyo wace molingana ndi zofunikira mu chibvomerezoci kopanda tsankho liri lonse monga la mtundu, khungu, kukhala mwamuna kapena mkazi, cilankhulidwe, cuma kapena maonekedwe ena ace onse.
Ndiponso tsankho lina liri lonse monga la malire a maiko, ndale kapena malo opezeka maikowo mosayang' ana pa ulamuliro wace wa dzikolo pai nkhani za ufulu kapena kayendetsedwe ka ulamuliro wace.
Munthu aliyense ali nao ufulu wapa umoyo m' makhalidwe ace onse mocinjirizidwa.
Palibe munthu amene adzakhala monga kapolo kapena kugwira nchito yopanda malipiro mokakamizidwa; Ukapolo kapena cibalo sizidzaloledwa ngakhale pang' ono.
Palibe munthu aliyense amene adzayenera kuzunzidwa mu njira iriyonse pa nthawi ya moyo wace.
Munthu aliyense ali obvomerezedwa mu umoyo wace wa umunthu molingana ndi lamulo loyang' ana pa makhalidwe a munthu.
Anthu onse ali olingana m' makhalidwe a umoyo wao kotero kuti palibe kusiyana kuli konse mu lamulo la kasamalidwe ka umoyo wao. Motero munthu aliyense ali nalo danga lokhala ndi cisamaliro coyenera molingana ndi chibvomerezo ca lamulo losamalira khalidwe la umoyo wa munthu aliyense.
Munthu aliyense ali nalo danga lodandaula pa khalidwe la umoyo wace ku mabungwe akulu-akulu oyang' ana pa madandaulo osiyana-siyana mu dziko malinga ndi ufulu wa munthu aliyense opatsidwa mwa lamulo pa umoyo wace.
Munthu aliyense sayenera kumangidwa, kusungidwa mu ndende kapena kuthamangitsidwa mu dziko lace mosayenera.
Munthy aliyense ali ndi danga lopereka dandaulo lace lokhudza za ufulu wa moyo wace ku bungwe la padera la cilungamo pofuna kulandira ciweruzo coyenera pa mlandu uli onse umene munthu angapezeke nao.
Munthu aliyense ayenera kulemekezedwa pa umoyo wace wa mseri (private life), banja kapena nyumba yace ndiponso umoyo wina wa iye yekha, mwinanso kudzudzulidwa pa khalidwe la umoyo wace wa mseri. Aliyense ali nalo danga locinjirizidwa ku khalidwe losokoneza umoyo wace mwa lamulo.
Munthu aliyense ali ndi danga lokhala ndi maganizo, nzeru kapena mpingo wa kukhosi kwace; ufuluwu ndi osintha mpingo kapena cipembedzo cace ndiponso ufulu wofalitsa nchito ndi cikhulupiliro ca mpingo mwa iye yekha kapena mogwirizana ndi anzace kupsyolera m' maphunziro, kacitidwe ka zinthu, cipembedzo ndiponso mu kaonekedwe ka nchitoyo.
Munthu aliyense ali ndi danga la ufulu wa maganizo ndi malankhulidwe; ufuluwu ukhudza maganizo a munthu kopanda msokonezo wina wace, kupempha ndi kulandira nzeru ndiponso kuphunzitsa ena nzeru kapena maganizo mogwiritsa nchito njira iriyonse.
Munthu aliyense pokhala nzika ya dziko ali ndi danga lolandira citetezo pa nchito za cisangalalo ca moyo wace ndi kuti ayenera kuzindikira za ufulu wace pa nchito za cuma, cisangalalo ndi miyambo cinthu comwe ciri cofunikira kwambiri pa ubwino ndi citukuko ca moyo wace.
Munthu aliyense ali ndi danga lopeza mpumulo ndi cisangalalo mwakupatsidwa maola okwanira ogwiliramo nchito ndi masiku a chuti ca malipiro.
Munthu aliyense ali nalo danga kapena ufulu wa cisangalalo ca moyo wace molingana ndi chibvomerezo ca zofuna za lamulo losamalira khalidwe la umoyo wa munthu.
Zosindikizidwa zonse za chibvomerezo ca lamulo losamalira khalidwe la umoyo wa munthu, sizitanthauza kuti Boma, kagulu ka anthu kapena munthu wina aliyense ali ndi danga kapena ufulu ocita zinthu zina zonse zofuna kuononga cilingo ca chibvomerezoci ai.
|